Marko 13:9 - Buku Lopatulika
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu ku bwalo la akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.
Onani mutuwo
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.
Onani mutuwo
“Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao.
Onani mutuwo
“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine.
Onani mutuwo