Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
Marko 13:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adayamba kuŵauza kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani kuti wina asakunyengeni. |
Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.
Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?
Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.