Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.
Marko 13:30 - Buku Lopatulika Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. |
Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.
Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.
chomwecho inunso, pamene muona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.
Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.