Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake.
Marko 13:12 - Buku Lopatulika Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana azidzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. |
Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake.
Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo.
Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake.
Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.
Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.
Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani.