Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Marko 13:10 - Buku Lopatulika Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nkofunika kuti Uthenga Wabwino uyambe walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. |
Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.
mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;
ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.
umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m'choonadi;
Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;