Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 12:5 - Buku Lopatulika

Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Munthuyo adatumanso wantchito wina, uyu ndiye adangomupheratu. Adachita chimodzimodzi ndi antchito ena ambiri, ena adaŵamenya, ena kuŵapheratu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.

Onani mutuwo



Marko 12:5
11 Mawu Ofanana  

Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.


ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.


Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi.


Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga.


Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.


Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.