Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?
Marko 12:3 - Buku Lopatulika Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namchotsa wopanda kanthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namchotsa wopanda kanthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma alimiwo adamugwira wantchitoyo nammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. |
Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?
pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.
Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.
Nati iye, Ndachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele ataya chipangano chanu, nagumula maguwa la nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.
ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.
Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.
koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.
Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali mu Chipata cha Benjamini cha kumtunda, chimene chinali kunyumba ya Yehova.
Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.
Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.
Ndipo m'nyengo yake anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wampesa.
Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi.
Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;
amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse;