Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.
Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;
amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale cholowa chanu ndilo dziko lodetsedwa mwa chidetso cha anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga ina kufikira nsonga inzake ndi utchisi wao.
Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.
Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?
Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu.