Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.
Marko 12:16 - Buku Lopatulika Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adampatsadi ndalamayo. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?” Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” |
Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri.
Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye.
Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.