Marko 12:12 - Buku Lopatulika Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene akulu a Ayuda aja adazindikira kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo, adafunitsitsa kumugwira, koma ankaopa khamu la anthu. Tsono adangomusiya nachokapo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita. |
Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.
Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.