Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.
Marko 12:11 - Buku Lopatulika Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ambuye Mulungu ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ambuye achita zimenezi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ” |
Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino.
Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.
Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.
Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenge konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu?
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.