Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Marko 11:9 - Buku Lopatulika Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anafuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anafuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amene adaali patsogolo, ndi amene adaali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti, “Hosana! “Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!” |
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.
anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele.
Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.