nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.
Marko 11:4 - Buku Lopatulika Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira aja adapitadi, nakapeza mwanawabuluyo ali chimangirire pa khomo m'mbali mwa mseu, ndipo adayamba kummasula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula, |
nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine.
Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.