Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Marko 11:3 - Buku Lopatulika Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wina akakakufunsani kuti, ‘Inu, nchiyani chimenecho?’ Inu mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito, akangothana naye amtumiza konkuno nthaŵi yomweyo.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’ ” |
Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu.
Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.
nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.
Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye.
Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere.
Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,
Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)
satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.