Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, paphiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake,
Marko 11:2 - Buku Lopatulika nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. |
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, paphiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake,
Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno.