Marko 11:11 - Buku Lopatulika Ndipo Iye analowa mu Yerusalemu, mu Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu ataloŵa m'Yerusalemu, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayang'anayang'ana zonse. Tsono poti chisisira chinali chitagwa, adatuluka napita ku Betaniya pamodzi ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. |
Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.