Marko 10:51 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?” Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.” |
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Chifukwa chake inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye mu Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi.
Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.