Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.
Marko 10:44 - Buku Lopatulika ndipo aliyense amene afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo amene aliyense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. |
Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.
Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;
Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.
Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.