Marko 10:41 - Buku Lopatulika Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakobeyo ndi Yohaneyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane. |
Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo.
Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?