Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.
Marko 10:21 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atamuyang'ana, adamkonda nkumuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.” |
Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banja la atate wake.
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.
Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri.
Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.
koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.
Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.
Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.
Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.
Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.
Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.
Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.