Marko 10:18 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. |
Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.
Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.
onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.