Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Marko 10:11 - Buku Lopatulika Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. |
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.
Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.
Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.