Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo;
Marko 10:10 - Buku Lopatulika Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za chinthu ichi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za chinthu ichi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adaloŵanso m'nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi. |
Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo;
Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinathe ife kuutulutsa?
Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?