Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.
Marko 1:43 - Buku Lopatulika Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, |
Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense.
nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.
Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.
Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika.