Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 1:39 - Buku Lopatulika

Ndipo analowa m'masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono adapita nalalika m'nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.

Onani mutuwo



Marko 1:39
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa.


Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye.


Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imeneyi.


Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala.


Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.


Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.


Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.