Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.
Marko 1:30 - Buku Lopatulika Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apongozi a Simoni anali gone, akudwala malungo, ndipo nthaŵi yomweyo anthu adamufotokozera za matendawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. |
Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo.
Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.
ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.
nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.
Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?