Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.
Marko 1:23 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'nyumba yamapempheroyo mudaaloŵa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuŵa kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, |
Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza.
Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.
Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.
Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.
Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa,
Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.
Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.