Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
Marko 1:17 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” |
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.
ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.