Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
Marko 1:13 - Buku Lopatulika Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira. |
Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.
Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu
Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a chipangano.
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.
Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani.
Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.