Ndinali mkupuma, koma anandithyola; inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; nandiimika ndikhale chandamali.
Maliro 3:3 - Buku Lopatulika Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake monditsutsa tsiku lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake monditsutsa tsiku lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoonadi adandikantha ndi dzanja lake, ankachita zimenezi mobwerezabwereza tsiku lonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero zoonadi anandikantha ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse. |
Ndinali mkupuma, koma anandithyola; inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; nandiimika ndikhale chandamali.
Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza.
ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa, popeza ndinaona thandizo langa kuchipata;
Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:
Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.