Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.
Malaki 3:9 - Buku Lopatulika Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinu otembereredwa nonsenu, mtundu wanu wonse, chifukwa choti mumandibera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. |
Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.
Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira padziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili.
Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima.
Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m'choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera gulu lonse la Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake.