Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Malaki 1:5 - Buku Lopatulika

Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Inu, Aisraele, mudzaziwona zimenezi ndi maso anu. Inu nomwe mudzati, “Ukulu wa Chauta umafika ngakhale kunja kwa malire a Aisraele.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Inu mudzaziona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati, ‘Yehova ndi Wamkulu, ukulu wake umafika ngakhale kunja kwa malire a Israeli!’

Onani mutuwo



Malaki 1:5
14 Mawu Ofanana  

Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale chodabwitsa ndi chotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu.


ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao.


Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo iwo okhala m'mizinda ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri;


Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, mu ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi.


Koma maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita.


Maso anu anapenya chochita Yehova chifukwa cha Baala-Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala-Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu.


Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.


Chifukwa chake tsono, imani pano, muone chinthu ichi chachikulu Yehova adzachichita pamaso panu.