Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.
Machitidwe a Atumwi 9:7 - Buku Lopatulika Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amene anali naye pa ulendowo adaima, atangoti chete. Mauwo ankaŵamva, koma osaona munthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu amene anali naye paulendo, anasowa chonena; iwo anamva mawu koma sanaone wina aliyense. |
Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala.
Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye.