Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 9:1 - Buku Lopatulika

Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Saulo uja ankaopsezabe ophunzira a Ambuye, nkumafuna kuŵapha. Adapita kwa mkulu wa ansembe onse

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe,

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 9:1
10 Mawu Ofanana  

Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa.


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende.


Pakuti ine ndili wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu.


Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,


monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine.


ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;