Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
Machitidwe a Atumwi 8:34 - Buku Lopatulika Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo nduna ija idati, “Pepani, tandiwuzani, kodi zimenezi mneneriyo akunena za yani, za iye mwini, kapena za wina?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, “Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?” |
Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;
M'kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa; mbadwo wake adzaubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake.