Machitidwe a Atumwi 7:7 - Buku Lopatulika Ndipo mtundu umene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adatinso, ‘Koma Ine ndidzaulanga mtundu wa anthuwo umene udzazisandutsa akapolo. Bwino lake zidzatuluka m'dzikomo nkudzandipembedza pamalo pano.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anati, ‘Ine ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo, ndipo pambuyo pake akadzatuluka mʼdzikolo adzandipembedza Ine pamalo pano.’ |
Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.