Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
Machitidwe a Atumwi 7:6 - Buku Lopatulika Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu adati, ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo ku dziko lina kumene eniake adzaziyesa akapolo, nadzazizunza pa zaka mazana anai.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anayankhula motere kwa iye: ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo, ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400.’ |
Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.