Iye ananding'amba m'kundida kwake, nakwiya nane, anandikukutira mano; mdani wanga ananditong'olera maso ake.
Machitidwe a Atumwi 7:54 - Buku Lopatulika Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene abwalo aja adamva mau a Stefanowo, adakwiya kwabasi, namchitira tsinya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano. |
Iye ananding'amba m'kundida kwake, nakwiya nane, anandikukutira mano; mdani wanga ananditong'olera maso ake.
Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.
Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.
Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano.
nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja.