Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.
Machitidwe a Atumwi 7:53 - Buku Lopatulika inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunge. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mudaalandira Malamulo a Mulungu kudzera mwa angelo, komabe simudaŵasunge konse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.” |
Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.
Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji?
Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;
Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe.
Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu.
Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.
Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,