Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 7:47 - Buku Lopatulika

Koma Solomoni anammangira nyumba.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Solomoni anammangira nyumba.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Solomoni ndiye adammangira nyumbayo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma anali Solomoni amene anamanga nyumbayo.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 7:47
10 Mawu Ofanana  

Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.


Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.


Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.


Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwake, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano la Yehova likhala m'nsalu zotchinga.


Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.