Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 7:41 - Buku Lopatulika

Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono masiku amenewo iwo adapanga fano la mwanawang'ombe. Adapereka nsembe kwa fanoli, nakondwerera ntchito za manja ao.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iyi ndi nthawi imene anapanga fano la mwana wangʼombe. Anapereka nsembe kwa fanoli nachita chikondwerero kulemekeza ntchito ya manja awo.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 7:41
11 Mawu Ofanana  

Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu;


Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse.


Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.


Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;