Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 7:40 - Buku Lopatulika

nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa mu Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m'Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho adauza Aroni kuti, ‘Tipangireni milungu kuti izititsogolera, pakuti sitikudziŵa chimene chamgwera Mose uja, amene adatitsogolera potuluka m'dziko la Ejipito.’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anati kwa Aaroni, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitsogolera kutuluka mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 7:40
2 Mawu Ofanana  

Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.


Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.