Ndipo Israele anakhala m'dziko la Ejipito, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nachuluka kwambiri.
Machitidwe a Atumwi 7:17 - Buku Lopatulika Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka mu Ejipito, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m'Ejipito, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pamene idayandikira nthaŵi yakuti Mulungu achite zimene adaalonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu udakula ndi kuchuluka ku Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nthawi itayandikira yakuti Mulungu achite zimene analonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu unakula ndi kuchuluka kwambiri mu Igupto. |
Ndipo Israele anakhala m'dziko la Ejipito, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nachuluka kwambiri.
Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu.
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.
Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai.