Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.
Machitidwe a Atumwi 7:11 - Buku Lopatulika Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani yense, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeze chakudya makolo athu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeza chakudya makolo athu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mudadzaloŵa njala m'dziko lonse la Ejipito, ndiponso m'Kanani, kotero kuti anthu adazunzika kwambiri. Makolo athu omwe sadathe kupeza chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya. |
Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.
ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.
Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni.