Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.
Machitidwe a Atumwi 7:1 - Buku Lopatulika Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mkulu wa ansembe onse adafunsa Stefano kuti, “Kodi zimenezi nzoona?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mkulu wa ansembe anafunsa Stefano kuti, “Kodi zimene akukunenerazi ndi zoona?” |
Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.
Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye mu Mesopotamiya, asanayambe kukhala mu Harani;