Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
Machitidwe a Atumwi 6:2 - Buku Lopatulika Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono atumwi khumi ndi aŵiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, naŵauza kuti, “Sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang'anira za chakudya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Atumwi khumi ndi awiriwo anasonkhanitsa ophunzira onse pamodzi ndipo anati, “Nʼkosayenera kuti ife tisiye kulalikira Mawu a Mulungu ndi kuyangʼanira za chakudya. |
Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?
Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze.
Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;
Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.
Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.
Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.