Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
Machitidwe a Atumwi 5:6 - Buku Lopatulika Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono achinyamata adabwera namkulunga m'nsalu. Adamnyamula nakamuika m'manda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda. |
Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.