Machitidwe a Atumwi 5:23 - Buku Lopatulika nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adati, “Takapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndipo alonda ali chilili pa makomo, koma titatsekula zitseko, sitidapezemo munthu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti, “Tinakapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndi alonda atayimirira pa khomo, koma pamene tinatsekula zitseko, sitinapezemo munthu aliyense mʼkatimo.” |
Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.