Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;
Machitidwe a Atumwi 4:8 - Buku Lopatulika Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adaŵayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Petro wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anawawuza kuti, “Inu olamulira ndi akulu! |
Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Koma panali m'mawa mwake, anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi;
Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,