Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Machitidwe a Atumwi 4:5 - Buku Lopatulika

Koma panali m'mawa mwake, anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma panali m'mawa mwake, anasonkhana pamodzi m'Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

M'maŵa mwake atsogoleri a Ayuda, akulu ao, ndiponso aphunzitsi a Malamulo adasonkhana ku Yerusalemu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mmawa mwake olamulira, akulu ndi aphunzitsi a malamulo anasonkhana mu Yerusalemu.

Onani mutuwo



Machitidwe a Atumwi 4:5
12 Mawu Ofanana  

Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu mu Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;


Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao,


Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane,


ndi kuti ansembe aakulu ndi akulu athu anampereka Iye ku chiweruziro cha imfa, nampachika Iye pamtanda.


Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu,


Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.


Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,